Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 8:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Muzikumbukira Yehova Mulungu wanu, chifukwa ndiye amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbirira makolo anu, monga mmene wachitira lero.+

  • Deuteronomo 28:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Yehova adzakutsegulira kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatse mvula pa nyengo yake+ m’dziko lako ndi kuti adalitse ntchito iliyonse ya manja ako.+ Udzakongoza mitundu yambiri koma iwe sudzakongola kanthu kwa iwo.+

  • 2 Mbiri 1:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 upatsidwa nzeru ndi luntha lodziwa zinthu.+ Ndikupatsanso katundu, chuma, ndi ulemu zochuluka kwambiri kuposa zimene anali nazo mafumu amene anakhalako iwe usanakhale,+ ndiponso zoposa zimene aliyense wobwera pambuyo pako adzakhale nazo.”+

  • Yobu 42:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Yehova anadalitsa+ kwambiri mapeto a Yobu kuposa chiyambi chake+ moti iye anakhala ndi nkhosa 14,000, ngamila 6,000, ng’ombe 2,000 zimene zinkagwira ntchito zili ziwiriziwiri, ndi abulu aakazi 1,000.

  • Miyambo 10:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa,+ ndipo sawonjezerapo ululu.+

  • 2 Akorinto 9:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Mulungu akukudalitsani m’njira iliyonse kuti muthe kupereka mowolowa manja m’njira zosiyanasiyana, ndipo kudzera m’zochita zathu, kuwolowa manja koteroko kukuchititsa anthu kuyamika Mulunguyo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena