1 Samueli 18:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Tsiku lotsatira,+ mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa Sauli,+ moti anayamba kuchita zinthu ngati mneneri+ m’nyumba mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kuimba nyimbo+ ngati kale ndipo Sauli anali ndi mkondo m’manja mwake.+ 1 Samueli 19:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Ndiyeno mzimu woipa wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa Sauli ali m’nyumba mwake, atatenga mkondo m’manja mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kumuimbira nyimbo. Yobu 34:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake. Yobu 34:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ndithudi, Mulungu sachita zoipa,+Ndipo Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.+ Aroma 2:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Iye adzaweruza aliyense malinga ndi ntchito zake motere:+ Aheberi 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+ Yakobo 1:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Munthu akakhala pa mayesero+ asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.
10 Tsiku lotsatira,+ mzimu woipa wochokera kwa Mulungu unayamba kugwira ntchito pa Sauli,+ moti anayamba kuchita zinthu ngati mneneri+ m’nyumba mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kuimba nyimbo+ ngati kale ndipo Sauli anali ndi mkondo m’manja mwake.+
9 Ndiyeno mzimu woipa wa Yehova+ unayamba kugwira ntchito pa Sauli ali m’nyumba mwake, atatenga mkondo m’manja mwake. Pa nthawiyi, Davide anali kumuimbira nyimbo.
11 Pakuti iye amapereka mphoto kwa munthu wochokera kufumbi malinga ndi zochita zake,+Ndipo amam’bweretsera zinthu zogwirizana ndi njira yake.
12 Chenjerani abale, kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+
13 Munthu akakhala pa mayesero+ asamanene kuti: “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.