2 Samueli 7:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pamenepo Mfumu Davide inabwera ndi kukhala pansi pamaso pa Yehova, ndipo inati: “Ndine yani ine,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa? Ndipo nyumba yanga n’chiyani kuti mundifikitse pamene ndili pano? Miyambo 15:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Kuopa Yehova ndi kumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+ ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+ Miyambo 18:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+ ndipo asanapeze ulemerero, amadzichepetsa.+ Miyambo 22:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Zotsatirapo za kudzichepetsa ndiponso kuopa Yehova ndizo chuma, ulemerero, ndi moyo.+ Yakobo 4:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+ 1 Petulo 5:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Choncho dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.+
18 Pamenepo Mfumu Davide inabwera ndi kukhala pansi pamaso pa Yehova, ndipo inati: “Ndine yani ine,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa? Ndipo nyumba yanga n’chiyani kuti mundifikitse pamene ndili pano?
33 Kuopa Yehova ndi kumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+ ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+
6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+