8 Anawauza kuti: “Bwererani kumahema anu ndi chuma chambiri ndiponso ziweto zambiri, ndi siliva, golide, mkuwa, zitsulo, ndi zovala zambiri.+ Tengani katundu amene munafunkha+ kwa adani anu n’kugawana ndi abale anu.”
22 Tsopano atumiki a Davide ndi Yowabu, anali kuchokera kunkhondo, atafunkha+ zinthu zambiri. Koma Abineri sanali ndi Davide ku Heburoni popeza anali atanyamuka mwamtendere ndipo anali pa ulendo wake.