-
2 Samueli 18:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Pamapeto pake, Abisalomu anakumana ndi atumiki a Davide. Abisalomu anali atakwera nyulu,* ndipo nyuluyo inadutsa paziyangoyango za nthambi za mtengo waukulu kwambiri. Choncho mutu wa Abisalomu unakola muziyangoyango za mtengo waukuluwo moti anali lendelende,+ koma nyulu imene anakwerapo ija inadutsa.
-