20Beni-hadadi+ mfumu ya Siriya anasonkhanitsa gulu lake lonse lankhondo ndiponso mahatchi+ ndi magaleta.+ Atatero ananyamuka pamodzi ndi mafumu ena 32,+ n’kupita kukazungulira+ mzinda wa Samariya+ kuti amenyane nawo.
24 Kenako mfumu ya Asuri inatenga anthu kuchokera ku Babulo,+ Kuta, Ava,+ Hamati,+ ndi Sefaravaimu+ n’kuwakhazika m’mizinda ya Samariya,+ m’malo mwa ana a Isiraeli. Anthuwo anatenga Samariya n’kumakhala m’mizinda yake.
6“Tsoka kwa anthu amene akukhala mwamtendere+ mu Ziyoni ndiponso anthu amene akumva kuti ndi otetezeka m’phiri la Samariya. Iwo ndiwo anthu olemekezeka a mtundu wotchuka pakati pa mitundu ina, ndipo nyumba yonse ya Isiraeli imabwera kwa anthu amenewa.