14 Amtokomawo+ anathamanga ndi kupita mofulumira atakwera pamahatchi amene anali kuwagwiritsa ntchito potumikira mfumu. Anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndipo lamulo linachokera m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+
13 Iwe mkazi wokhala ku Lakisi,+ mangirira galeta ku gulu la mahatchi.* Mzinda umenewu ndiwo unayambitsa tchimo la mwana wamkazi wa Ziyoni,+ pakuti kupanduka kwa Isiraeli kwapezeka mwa iwe.+