Ekisodo 25:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndipo mundipangire malo opatulika, popeza ndiyenera kukhala pakati panu.+ Levitiko 26:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Motero ndidzayendadi pakati panu ndi kukusonyezani kuti ine ndine Mulungu wanu,+ ndipo inu mudzakhala anthu anga.+ Salimo 132:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Yehova wasankha Ziyoni,+Ndipo amafunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye amati:+ 2 Akorinto 6:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+ Chivumbulutso 21:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema+ cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo,+ ndipo iwo adzakhala anthu ake.+ Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.+
12 Motero ndidzayendadi pakati panu ndi kukusonyezani kuti ine ndine Mulungu wanu,+ ndipo inu mudzakhala anthu anga.+
16 Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Pakuti ifeyo ndife kachisi+ wa Mulungu wamoyo, monga ananenera Mulungu kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndi kuyenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+
3 Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu, akuti: “Taonani! Chihema+ cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo,+ ndipo iwo adzakhala anthu ake.+ Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo.+