27 Kenako anaika akerubiwo m’chipinda chamkati, ndipo mapiko awo anali otambasula.+ Nsonga ya phiko la kerubi mmodzi inagunda khoma ndipo nsonga ya phiko la kerubi winayo inagundanso khoma lina. Mapiko awo anafika pakati pa nyumbayo, ndipo anagundana.+