5 dziko la Agebala+ ndiponso dziko lonse la Lebanoni, kotulukira dzuwa, kuyambira ku Baala-gadi+ m’munsi mwa phiri la Herimoni mpaka kumalire ndi Hamati.+
25 Yerobowamu ndiye anabwezeretsa malire a Isiraeli kuyambira kumalire ndi Hamati+ mpaka kunyanja ya Araba.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi mawu a Yehova Mulungu wa Isiraeli omwe anawalankhula kudzera mwa mtumiki wake Yona+ mwana wa Amitai, mneneri amene anachokera ku Gati-heferi.+
14 Tsopano Yehova, Mulungu wa makamu wanena kuti, ‘Inu a m’nyumba ya Isiraeli, ine ndikukudzutsirani mtundu wa anthu+ umene udzakuponderezani kuyambira kumalire ndi Hamati+ mpaka kuchigwa cha Araba.’”