Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 96:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+

      Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+

  • Salimo 135:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva ndi golide,+

      Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi.+

  • Yesaya 44:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Anthu onse opanga zifaniziro zosema ndi opanda pake,+ ndipo mafano awo okondedwa adzakhala opanda phindu.+ Monga mboni zawo, mafanowo saona chilichonse ndipo sadziwa chilichonse,+ kuti anthu opanga mafanowo achite manyazi.+

  • Yeremiya 10:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ali ngati choopsezera mbalame m’munda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+ Iwo amachita kunyamulidwa ndithu chifukwa sangathe kuyenda okha.+ Mafano musamachite nawo mantha chifukwa sangakuvulazeni, ndipo kuwonjezera pamenepo, sangachite chabwino chilichonse.”+

  • Mika 4:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake.+ Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu+ mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.+

  • Aroma 1:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 ndipo anasandutsa ulemerero+ wa Mulungu amene sawonongeka kukhala ngati chifaniziro+ cha munthu, mbalame, zolengedwa za miyendo inayi ndi zokwawa,+ zonsezo zimene zimawonongeka.

  • 1 Akorinto 8:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno pa nkhani ya kudya+ zakudya zoperekedwa kwa mafano, timadziwa kuti fano ndi lopanda pake+ m’dziko, ndiponso kuti kulibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena