2 Mbiri 16:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+ Yeremiya 23:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova. Aheberi 4:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+ 1 Petulo 3:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+
9 Pajatu maso a Yehova+ akuyendayenda padziko lonse lapansi+ kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo+ uli wathunthu kwa iye. Mwachita zopusa+ pankhani imeneyi, chifukwa kuyambira tsopano anthu azichita nanu nkhondo.”+
24 “Kodi munthu aliyense angabisale m’malo obisika ine osamuona?”+ watero Yehova. “Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene chingabisike kwa ine?”+ watero Yehova.
13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino. Ndipotu ife tikuyenera kudzayankha pa zochita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.+
12 Pakuti maso+ a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo,+ koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”+