33 Malo otchedwa Tofeti*+ owonongerako Asuri akonzedwa kale. Malowo akonzedweranso mfumu yawo.+ Malo amene iye wakonzawo ndi ozama ndipo kuli moto waukulu ndi nkhuni zambiri. Mpweya wa Yehova ukuyatsa malowo ngati mtsinje wa sulufule.+
31 Iwo amanga malo okwezeka ku Tofeti,+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ kuti azitentha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuchita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’+