Yeremiya 32:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ukuloseranso kuti, ‘Mfumu ya Babulo idzatenga Zedekiya kupita naye ku Babulo ndipo adzakhala komweko kufikira nditamucheukira,’+ watero Yehova. Ukunenanso kuti, ‘ngakhale kuti anthu inu mukupitiriza kumenyana ndi Akasidi simudzapambana.’ N’chifukwa chiyani ukulosera zimenezi?”+ Yeremiya 34:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Iweyo sudzazemba kuti asakugwire chifukwa adzakugwira ndithu ndi kukupereka m’manja mwake.+ Udzaonana ndi mfumu ya Babulo+ maso ndi maso, ndipo idzalankhula nawe ndi kupita nawe ku Babulo.’ Ezekieli 17:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, “Pali ine Mulungu wamoyo,+ munthu amene ananyoza lumbiro+ ndi kuphwanya pangano limene anachita ndi mfumu imene inamulonga ufumu, adzafera m’dziko la mfumu yomweyo, dziko la Babulo.+
5 Ukuloseranso kuti, ‘Mfumu ya Babulo idzatenga Zedekiya kupita naye ku Babulo ndipo adzakhala komweko kufikira nditamucheukira,’+ watero Yehova. Ukunenanso kuti, ‘ngakhale kuti anthu inu mukupitiriza kumenyana ndi Akasidi simudzapambana.’ N’chifukwa chiyani ukulosera zimenezi?”+
3 Iweyo sudzazemba kuti asakugwire chifukwa adzakugwira ndithu ndi kukupereka m’manja mwake.+ Udzaonana ndi mfumu ya Babulo+ maso ndi maso, ndipo idzalankhula nawe ndi kupita nawe ku Babulo.’
16 “‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, “Pali ine Mulungu wamoyo,+ munthu amene ananyoza lumbiro+ ndi kuphwanya pangano limene anachita ndi mfumu imene inamulonga ufumu, adzafera m’dziko la mfumu yomweyo, dziko la Babulo.+