25 Patapita nthawi, mu Samariya+ munagwa njala yaikulu. Asiriyawo anapitirizabe kuzungulira mzindawo mpaka mtengo wogulira mutu wa bulu+ unafika pa ndalama 80 zasiliva, ndipo zitosi za nkhunda+ zodzaza manja awiri mtengo wake unafika pa ndalama zisanu zasiliva.