10 Kuwonjezera apo, Yoswa anabwerera ndi kukalanda+ mzinda wa Hazori+ n’kupha mfumu yake ndi lupanga.+ Anachita zimenezi chifukwa mzinda wa Hazori unali likulu la maufumu onsewa.
2 Choncho Yehova anawagulitsa+ kwa Yabini mfumu yachikanani, imene inali kulamulira ku Hazori.+ Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera,+ yemwe anali kukhala ku Haroseti-ha-goimu.+