21 Iwo anabweretsa ng’ombe zamphongo 7,+ nkhosa zamphongo 7, ana a nkhosa amphongo 7 ndi mbuzi zamphongo 7 kuti azipereke monga nsembe yamachimo+ ya ufumuwo, ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Chotero Hezekiya anauza ana a Aroni, omwe anali ansembe,+ kuti apereke nsembeyo paguwa lansembe la Yehova.