13 Pamenepo Gadi anapita kwa Davide ndi kumuuza kuti:+ “Kodi m’dziko lanu mubwere njala yaikulu zaka 7,+ kapena muzithawa adani anu akukuthamangitsani miyezi itatu,+ kapena kodi kugwe mliri wa masiku atatu m’dziko lanu?+ Ganizirani mofatsa zoti ndikayankhe kwa Amene wandituma.”