17 Pamene amuna a mzindawo anatuluka kudzamenyana ndi Yowabu, ena mwa anthu, atumiki a Davide anakanthidwa ndi kugwa, ndipo Uriya Mhiti nayenso anafa.+
9 N’chifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova mwa kuchita chinthu choipa+ pamaso pake? Uriya Mhiti unamupha ndi lupanga, ndipo mkazi wake unamutenga kukhala mkazi wako,+ pamene Uriyayo unamupha ndi lupanga+ la ana a Amoni.