Ekisodo 14:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Farao atafika pafupi, ana a Isiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Pamenepo ana a Isiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.+ 2 Mbiri 13:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ayudawo atatembenuka, anangoona kuti adani awo ali kumbuyo ndi kutsogolo kwawo.+ Choncho anayamba kufuulira Yehova+ pamene ansembe anali kuliza malipenga mokweza. Salimo 50:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pa tsiku la nsautso undiitane.+Ine ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.”+
10 Farao atafika pafupi, ana a Isiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Pamenepo ana a Isiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.+
14 Ayudawo atatembenuka, anangoona kuti adani awo ali kumbuyo ndi kutsogolo kwawo.+ Choncho anayamba kufuulira Yehova+ pamene ansembe anali kuliza malipenga mokweza.