4 Chifukwa cha kukhulupirika kwa Davide,+ Yehova Mulungu wake anam’patsa nyale+ mu Yerusalemu mwa kukweza mwana wake pambuyo pake, ndiponso kuchititsa kuti Yerusalemu akhalepobe.+
7 Koma Yehova sanafune kuwononga nyumba ya Davide+ chifukwa cha pangano+ limene anapangana ndi Davide, monga momwe anamuuzira kuti adzam’patsa+ nyale nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.+