-
2 Mafumu 14:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Yehoasi mfumu ya Isiraeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda mwana wa Yehoasi mwana wa Ahaziya ku Beti-semesiko. Kenako Yehoasi anatenga Amaziya n’kupita naye ku Yerusalemu, ndipo anakagumula mpanda wa Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efuraimu+ mpaka kukafika pa Chipata cha Pakona.+ Anagumula mpata waukulu mikono 400.*
-
-
Zekariya 14:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 “Dziko lonse lidzasintha ndi kukhala ngati chigwa cha Araba+ kuyambira ku Geba+ kukafika ku Rimoni+ kum’mwera kwa Yerusalemu. Mzindawu udzakwezedwa pamalo ake ndipo anthu adzakhalamo.+ Anthuwo adzakhalamo kuyambira ku Chipata cha Benjamini+ mpaka ku Chipata Choyamba, kukafika ku Chipata cha Pakona. Komanso adzakhala kuyambira ku Nsanja ya Hananeli+ mpaka kukafika kumalo a mfumu oponderamo mphesa.
-