27 Ndiyeno Basa+ mwana wa Ahiya wa nyumba ya Isakara, anayamba kuchitira chiwembu Nadabu. Iye anapha Nadabu kumzinda wa Gebetoni,+ womwe unali m’manja mwa Afilisiti, pa nthawi imene Nadabu ndi Aisiraeli onse anali kuukira Gebetoni.
25 Asilikaliwo atachoka (popeza anamusiya akuvutika kwambiri),+ atumiki ake anam’konzera chiwembu+ chifukwa cha magazi+ a ana a wansembe Yehoyada+ ndipo anamuphera pabedi+ lake. Kenako anamuika m’manda mu Mzinda wa Davide+ koma sanamuike m’manda a mafumu.+
27 Amaziya atasiya kutsatira Yehova, anthu anam’konzera chiwembu+ ku Yerusalemu. Patapita nthawi iye anathawira ku Lakisi.+ Koma anthuwo anatumiza anthu ena omwe anamutsatira ku Lakisiko n’kukamuphera komweko.+