10 Pamenepo mtumikiyo anatenga ngamila 10 pa ngamila za mbuye wake, n’kutenganso zabwino za mtundu uliwonse kwa mbuye wake zoti akazigwiritse ntchito.+ Kenako ananyamuka ulendo wopita ku Mesopotamiya, kumzinda wa Nahori.
6 Chikhamu cha ngamila zamphongo zing’onozing’ono za ku Midiyani ndi ku Efa+ chidzadzaza dziko lako. Anthu onse a ku Sheba+ adzabwera atanyamula golide ndi lubani. Iwo adzatamanda Yehova pamaso pa anthu onse.+