18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse,+ zazikulu+ ndi zazing’ono, za m’nyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma+ cha m’nyumba ya Yehova, chuma cha mfumu+ ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse n’kupita nacho ku Babulo.
19 Ziwiya+ zimene ukupatsidwa kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wa panyumba ya Mulungu wako, ukazipereke zonse ku Yerusalemu n’kukaziika pamaso pa Mulungu.+