2 Kenako Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi abale ake ansembe, ndiponso Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi abale ake, ananyamuka n’kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Isiraeli kuti aziperekerapo nsembe zopsereza, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa+ m’chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu woona.
11 Pa choperekacho ukatengepo siliva ndi golide n’kupangira chisoti chachifumu chaulemerero.+ Chisoticho udzaveke Yoswa+ mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki.