2 Kenako Sekaniya mwana wa Yehiela+ wochokera mwa ana a Elamu+ anauza Ezara kuti: “Ifeyo tachita zosakhulupirika kwa Mulungu wathu, chifukwa tinatenga akazi achilendo kuchokera kwa anthu a mitundu ina.+ Koma tsopano Aisiraeli ali ndi chiyembekezo+ pa nkhani imeneyi.