3Ndiyeno Eliyasibu+ mkulu wa ansembe ndi abale ake, ansembe, anayamba kumanga Chipata cha Nkhosa.+ Iwo anapatula mbali imeneyi+ ndi kuika zitseko zake. Anapatula mbali imeneyi mpaka ku Nsanja ya Meya+ ndi Nsanja ya Hananeli.+
39 Anadutsanso pamwamba pa Chipata cha Efuraimu,+ Chipata cha Mzinda Wakale,+ Chipata cha Nsomba+ mpaka kukafika pa Nsanja ya Hananeli,+ Nsanja ya Meya+ ndi ku Chipata cha Nkhosa,+ ndipo anaima pa Chipata cha Alonda.
2 Tsopano mu Yerusalemu pachipata cha nkhosa+ pali dziwe limene m’Chiheberi limatchedwa Betesida. M’mbali mwa dziwelo muli makonde asanu amene ali ndi zipilala.