11 Kenako Aleviwo adzakhala atumiki m’malo anga opatulika. Adzakhala ndi maudindo oyang’anira zipata za Nyumba ino ndipo adzakhala atumiki a pa Nyumbayi.+ Iwo azidzapha nyama za nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zina za anthu+ ndipo adzaimirira pamaso pa anthuwo ndi kuwatumikira.+