2 Choncho Ezara wansembe+ anabweretsa chilamulo pamaso pa mpingo+ wa amuna komanso akazi ndi ana onse amene akanatha kumvetsera ndi kuzindikira+ zimene zinali kunenedwa. Limeneli linali tsiku loyamba la mwezi wa 7.+
16 Kenako anabwera ku Nazareti,+ kumene analeredwa. Malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata, analowa m’sunagoge,+ ndi kuimirira kuti awerenge Malemba.