Numeri 23:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ndingathe bwanji kutemberera anthu amene Mulungu sanawatemberere?+Anthu amene Yehova sanawaitanire tsoka, ndingathe bwanji kuwaitanira tsoka?+ Numeri 24:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pamenepo Balaki anapsera mtima Balamu n’kuwomba m’manja.+ Kenako anauza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere+ adani anga, koma iwe wawadalitsa kwambiri katatu konseka! Deuteronomo 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+ Salimo 109:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Alekeni anditemberere,+Koma inu mundipatse madalitso.+Iwo aimirira kuti andiukire koma inu muwachititse manyazi,+Ndipo ine mtumiki wanu ndisangalale.+ Mika 6:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Inu anthu anga, chonde kumbukirani+ zimene Balaki mfumu ya Mowabu anakonza kuti achite+ ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+ Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+ Zimenezo zinachitika n’cholinga chakuti zochita za Yehova zolungama zidziwike.”+
8 Ndingathe bwanji kutemberera anthu amene Mulungu sanawatemberere?+Anthu amene Yehova sanawaitanire tsoka, ndingathe bwanji kuwaitanira tsoka?+
10 Pamenepo Balaki anapsera mtima Balamu n’kuwomba m’manja.+ Kenako anauza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere+ adani anga, koma iwe wawadalitsa kwambiri katatu konseka!
5 Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+
28 Alekeni anditemberere,+Koma inu mundipatse madalitso.+Iwo aimirira kuti andiukire koma inu muwachititse manyazi,+Ndipo ine mtumiki wanu ndisangalale.+
5 Inu anthu anga, chonde kumbukirani+ zimene Balaki mfumu ya Mowabu anakonza kuti achite+ ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+ Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+ Zimenezo zinachitika n’cholinga chakuti zochita za Yehova zolungama zidziwike.”+