7Pambuyo pa zimenezi, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita+ ya ku Perisiya, panali mwamuna wina dzina lake Ezara.+ Iye anali mwana wa Seraya.+ Seraya anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Hilikiya,+
2Ndiyeno tsiku lina m’mwezi wa Nisani,*+ m’chaka cha 20+ cha mfumu Aritasasita,+ mfumuyo inali kufuna vinyo. Pamenepo ine ndinatenga vinyoyo ndi kum’pereka kwa mfumu monga mwa nthawi zonse.+ Koma ndinali ndisanakhalepo wachisoni pamaso pake.+