17 Ndiyeno mfumu inakonda kwambiri Esitere kuposa akazi ena onse, moti mfumu inakondwera naye ndipo inamusonyeza kukoma mtima kosatha kuposa anamwali ena onse.+ Pamenepo mfumu inamuveka duku lachifumu kumutu kwake ndi kumusandutsa mfumukazi+ m’malo mwa Vasiti.