11 M’makalatawo mfumu inalola Ayuda amene anali m’mizinda yosiyanasiyana kuti asonkhane+ ndi kuteteza miyoyo yawo. Inawalolanso kuwononga, kupha ndi kufafaniza magulu onse ankhondo a anthu+ ndi zigawo zimene zinali kuwachitira nkhanza, ngakhalenso ana ndi akazi ndiponso kufunkha zinthu zawo.+