Esitere 4:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Moredekai+ anadziwa zonse zimene zinachitika.+ Choncho anang’amba zovala zake ndi kuvala chiguduli*+ ndipo anadzithira phulusa+ ndi kutuluka kupita pakati pa mzinda. Ndiyeno anayamba kulira mofuula ndiponso mopwetekedwa mtima.+ Salimo 65:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+ Salimo 142:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 142 Ndinafuulira Yehova kuti andithandize.+Ndinafuulira Yehova kuti andikomere mtima.+
4 Moredekai+ anadziwa zonse zimene zinachitika.+ Choncho anang’amba zovala zake ndi kuvala chiguduli*+ ndipo anadzithira phulusa+ ndi kutuluka kupita pakati pa mzinda. Ndiyeno anayamba kulira mofuula ndiponso mopwetekedwa mtima.+