4 Ndithu, Mulungu sanalekerere angelo+ amene anachimwa aja osawapatsa chilango, koma mwa kuwaponya mu Tatalasi,*+ anawaika m’maenje a mdima wandiweyani powasungira chiweruzo.+
9 Koma pamene Mikayeli+ mkulu wa angelo+ anasemphana maganizo+ ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose,+ sanayese n’komwe kumuweruza ndi mawu onyoza,+ m’malomwake anati: “Yehova akudzudzule.”+