8 Ndiyeno anthu onse anasonkhana pamodzi mogwirizana+ m’bwalo lalikulu+ limene linali pafupi ndi Chipata cha Kumadzi.+ Pamenepo anthuwo anauza Ezara+ wokopera Malemba kuti abweretse buku+ la chilamulo cha Mose+ limene Yehova analamula Aisiraeli kuti azilitsatira.+