11 Ndiyeno Yehova wanena kuti, ‘Taona, ndikukugwetsera tsoka m’nyumba yako yomwe.+ Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa mwamuna wina,+ ndipo iye adzagona ndi akazi ako anthu onse akuona.+
10 Choncho akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena, ndipo minda yawo ndidzaipereka kwa anthu ena.+ Pakuti kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu aliyense wa iwo akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+