Yobu 34:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Alipo amene sanakonderepo akalonga,Ndipo saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka,+Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+ Salimo 139:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Maso anu anandiona pamene ndinali mluza,+Ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa+Koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa. Miyambo 14:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Wobera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+ koma wokomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+ Miyambo 22:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Munthu wolemera ndiponso munthu wosauka n’chimodzimodzi.+ Amene anapanga onsewa ndi Yehova.+ Malaki 2:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 “Kodi tonsefe atate wathu si mmodzi?+ Kodi si Mulungu mmodzi amene anatilenga?+ N’chifukwa chiyani tikuchitirana zachinyengo,+ mwa kuipitsa pangano la makolo athu akale?+
19 Alipo amene sanakonderepo akalonga,Ndipo saganizira kwambiri wolemekezeka kuposa wonyozeka,+Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+
16 Maso anu anandiona pamene ndinali mluza,+Ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu.M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa+Koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.
31 Wobera munthu wosauka mwachinyengo amanyoza amene anamupanga,+ koma wokomera mtima munthu wosauka amalemekeza amene anamupanga.+
10 “Kodi tonsefe atate wathu si mmodzi?+ Kodi si Mulungu mmodzi amene anatilenga?+ N’chifukwa chiyani tikuchitirana zachinyengo,+ mwa kuipitsa pangano la makolo athu akale?+