52 Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Inde, iwo anapha+ amene analengezeratu za kubwera kwa Wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndi kumupha,+
12 osati ngati Kaini, amene anachokera kwa woipayo n’kupha+ m’bale wake. N’chifukwa chiyani iye anapha m’bale wake? Chifukwa chakuti zochita zake zinali zoipa,+ koma za m’bale wake zinali zolungama.+