4 Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndatumiza mpukutuwo kuti ukalowe m’nyumba ya munthu wakuba ndi m’nyumba ya munthu wolumbira mwachinyengo m’dzina langa.+ Mpukutuwo upita kukakhala m’nyumba mwake n’kuwonongeratu nyumbayo, matabwa ake ndi miyala yake.’”+