-
Yeremiya 20:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Pakuti ndinamva zoipa zimene ambiri anali kunena.+ Zinali zochititsa mantha paliponse. Iwo anali kunena kuti, “Fotokozani kuti ifenso tinene za iye.”+ Munthu aliyense anali kundiuza kuti “Mtendere!” koma anali kundiyang’anira kuti ndilakwitse chinachake+ ndipo anali kunena kuti: “Achita chinachake chopusa+ ameneyu ndipo timugonjetsa ndi kumubwezera.”
-