7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake,+ pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.+ Munthu amaona zooneka ndi maso,+ koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”+