2 Bwerera kwa Yehova ndi mawu osonyeza kulapa.+ Anthu nonsenu uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu.+ Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife, ndipo mawu apakamwa pathu akhale ngati ana amphongo a ng’ombe amene tikuwapereka nsembe kwa inu.+