Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 13:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Choncho, Loti anakweza maso ake n’kuona Chigawo* chonse cha Yorodano+ mpaka kukafika ku Zowari,+ ndipo anaona kuti chinali chigawo chobiriwira bwino. Chinali chobiriwira bwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Yehova+ komanso ngati mmene linalili dziko la Iguputo. Pa nthawiyi n’kuti Yehova asanawononge Sodomu ndi Gomora.

  • Genesis 19:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Iye anawononga mizindayi, ngakhale Chigawo chonsecho ndi anthu onse a m’mizindayi, kuphatikizapo zomera za panthaka.+

  • Deuteronomo 29:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Adzanena mawuwo akadzaonanso sulufule, mchere+ ndi kutentha,+ moti m’dzikomo simungabzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, mofanana ndi Sodomu ndi Gomora,+ Adima+ ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga mu ukali ndi mkwiyo wake.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena