Deuteronomo 28:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Anthu amene sunawadziwe adzadya zipatso za m’dziko lako ndi mbewu zako zonse.+ Motero udzakhala wodyeredwa ndi woponderezedwa nthawi zonse.+ Deuteronomo 28:51 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 51 Iwo adzadya chipatso cha ziweto zako ndi zipatso za nthaka yako kufikira utafafanizidwa,+ ndipo sadzakusiyirako mbewu, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ng’ombe yako kapena mwana wa nkhosa yako kufikira atakuwonongeratu.+ Oweruza 6:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Iwo anali kubwera ndi ziweto zawo ndi mahema awo. Anali kubwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Iwo anali kubwera m’dzikomo n’kumaliwononga.+
33 Anthu amene sunawadziwe adzadya zipatso za m’dziko lako ndi mbewu zako zonse.+ Motero udzakhala wodyeredwa ndi woponderezedwa nthawi zonse.+
51 Iwo adzadya chipatso cha ziweto zako ndi zipatso za nthaka yako kufikira utafafanizidwa,+ ndipo sadzakusiyirako mbewu, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ng’ombe yako kapena mwana wa nkhosa yako kufikira atakuwonongeratu.+
5 Iwo anali kubwera ndi ziweto zawo ndi mahema awo. Anali kubwera ochuluka kwambiri ngati dzombe,+ ndipo iwo ndi ngamila zawo anali osawerengeka.+ Iwo anali kubwera m’dzikomo n’kumaliwononga.+