Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 19:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pamenepo phiri la Sinai linafuka utsi ponseponse,+ chifukwa chakuti Yehova anatsikira paphiripo m’moto.+ Utsi wakewo unali kukwera kumwamba ngati utsi wa uvuni,+ ndipo phiri lonse linali kunjenjemera kwambiri.+

  • Ekisodo 20:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Ndiyeno anthu onse anali kumva mabingu ndi kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa ndipo anali kuona kung’anima kwa mphezi ndiponso phiri likufuka utsi. Anthuwo atamva ndi kuona zimenezi ananjenjemera ndipo anaimabe patali.+

  • Oweruza 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Yehova, pamene munayenda kuchokera ku Seiri,+

      Pamene munaguba kuchokera kudera la Edomu,+

      Dziko linagwedezeka,+ kumwamba kunagwetsa madzi,+

      Mitambo inagwetsa madzi.

  • Salimo 29:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Iye akuichititsa kudumphadumpha ngati mwana wa ng’ombe,+

      Lebanoni ndi Sirioni+ akudumphadumpha ngati ana a ng’ombe zakutchire.

  • Salimo 68:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Dziko lapansi linagwedezeka,+

      Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+

      Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+

  • Yeremiya 4:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Ndinaona mapiri ndipo anali kugwedezeka. Zitunda zonse zinali kunjenjemera.+

  • Habakuku 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Iye anaima chilili kuti agwedeze dziko lapansi.+ Anayang’ana mitundu ya anthu ndipo mitunduyo inadumpha.+

      Mapiri amuyaya anaphwanyidwa.+ Zitunda zimene zidzakhalapo mpaka kalekale* zinawerama.+ Zimenezi ndi njira zake zakalekale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena