Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 61:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Mfumuyo idzakhala pamaso pa Mulungu mpaka kalekale.+

      Isonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha ndi kuipatsa choonadi kuti zimenezi ziiteteze.+

  • Salimo 66:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Adalitsike Mulungu amene sananyalanyaze pemphero langa,

      Kapena kundimana kukoma mtima kwake kosatha.+

  • Salimo 89:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 89 Ndidzaimba mpaka kalekale za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+

      Ndidzalengeza ndi pakamwa panga ku mibadwomibadwo za kukhulupirika kwanu.+

  • Salimo 138:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  2 Ndidzawerama nditayang’ana kukachisi wanu woyera,+

      Ndipo ndidzatamanda dzina lanu+

      Chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha+ ndi choonadi chanu.+

      Pakuti malonjezo+ amene munawachita m’dzina lanu ndi aakulu ndithu. Koma kukwaniritsidwa kwa malonjezowo n’kwakukulu koposa.+

  • Mika 7:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Zonse zimene munanena kwa Yakobo zinali zoona ndipo Abulahamu munamusonyeza kukoma mtima kosatha. Ifenso mudzatichitira zomwezo chifukwa n’zimene munalonjeza makolo athu kalekale.+

  • Aroma 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ayi! Koma Mulungu akhale wonena zoona,+ ngakhale kuti munthu aliyense angapezeke kukhala wonama,+ monganso Malemba amanenera kuti: “Mukamalankhula mumalankhula zachilungamo, kuti mupambane pamene mukuweruzidwa.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena