Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Nehemiya 6:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Ndiyeno adani athu onse atangomva zimenezi,+ komanso anthu a mitundu ina yotizungulira ataona, anachita manyazi ndipo anadziwa kuti ntchito imeneyi yatheka chifukwa cha Mulungu wathu.+

  • Esitere 6:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Ndiyeno Hamani anafotokozera Zeresi+ mkazi wake ndi anzake onse chilichonse chimene chinam’chitikira. Pamenepo amuna anzeru+ amene anali kum’tumikira ndi Zeresi mkazi wake anati: “Ngati n’zoona kuti Moredekai amene iwe wayamba kugonja pamaso pake ndi Myuda, sudzamugonjetsa koma udzagonja ndithu pamaso pake.”+

  • Esitere 9:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndiyeno Ayuda anakantha adani awo onse ndipo anawapha ndi kuwawononga ndi lupanga.+ Ayudawo anachita zonse zimene anali kufuna kwa anthu amene anali kudana nawo.+

  • Yesaya 37:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika m’makutu mwanga.+

      Ndithu ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga, ndipo ndidzamanga zingwe zanga pakamwa pako.+

      Kenako ndidzakukoka n’kukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”+

  • Zekariya 12:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pa tsiku limenelo,+ Yerusalemu ndidzamusandutsa mwala wotopetsa+ kwa anthu a mitundu yonse. Onse onyamula mwala umenewo, ndithu adzatemekatemeka koopsa. Anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adzasonkhana pamodzi kuti amuukire.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena