Ekisodo 20:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Usapereke umboni wonamizira mnzako.+ Salimo 52:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Lilime lako limakonza chiwembu, ndipo ndi lakuthwa ngati lezala,+Limachita zachinyengo.+ Salimo 57:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Moyo wanga uli pakati pa mikango.+Sindingachitire mwina koma kugona pakati pa ana a anthu, amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,+Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+ Salimo 120:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Kodi iwe lilime lachinyengo,+Munthu adzakupatsa chiyani ndipo adzawonjezera chiyani pa iwe? Salimo 140:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Anola lilime lawo ndipo lakhala ngati la njoka.+M’milomo yawo muli poizoni wa mphiri.+ [Seʹlah.] Yeremiya 9:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Iwo amakunga lilime lawo ngati uta kuti aponye chinyengo,+ koma iwo si okhulupirika m’dzikoli. “Iwo anali kuchita zoipa motsatizanatsatizana ndipo anandinyalanyaza,”+ watero Yehova. Yakobo 3:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Lilimenso ndi moto.+ Mwa ziwalo zathu zonse, lilime ndilo lili lodzaza ndi zosalungama chifukwa limadetsa thupi lonse.+ Lili ndi moto wa Gehena* ndipo limayatsa moyo wonse wa munthu.
4 Moyo wanga uli pakati pa mikango.+Sindingachitire mwina koma kugona pakati pa ana a anthu, amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,+Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+
3 Iwo amakunga lilime lawo ngati uta kuti aponye chinyengo,+ koma iwo si okhulupirika m’dzikoli. “Iwo anali kuchita zoipa motsatizanatsatizana ndipo anandinyalanyaza,”+ watero Yehova.
6 Lilimenso ndi moto.+ Mwa ziwalo zathu zonse, lilime ndilo lili lodzaza ndi zosalungama chifukwa limadetsa thupi lonse.+ Lili ndi moto wa Gehena* ndipo limayatsa moyo wonse wa munthu.